Mafumu a m’boma la Zomba awayamikira kamba kogwirana manja ndi boma polimbana ndi nkhani zokhudza m’chitidwe wopopa magazi ndi nkhanza zomwe anthu a khungu la chi alubino akhala akukomana nazo m’bomalo.
Bwanamkubwa wa bomalo a Emmanuel Bambe, ndi omwe anena izi pa msonkhano wapakati pa adindo osiyanasiyana, apolisi ndi a bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) m’bomalo.
Pamenepa a Bambe alimbikitsa adindowa kuti apitilize kudzipereka pa ntchito zothandiza kubweletsa bata m’bomalo.
Polankhulapo, mkulu wa apolisi m’boma la Zomba, Senior Asistant Comissioner,Hestings Mathankiwayamikira mafumu komanso atolankhani kaamba kotengapo mbali pa ntchito yothetsa mphekeserazi.