Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MA BISHOPU AMPINGO WA ANGLICAN APEMPHA KAMPENI YA BATA

$
0
0

Pomwe mabungwe ndi zipembezo zikupitiriza kudzudzula mchitidwe wa ziwawa womwe unaphetsa wapolisi ndi munthu wamba m’modzi kwa Goliati mboma la Thyolo mpingo wa Anglican wapempha boma kuti lionetsetse kuti onse omwe akukhuzidwa ndi zipolowezi alandire chilango.

Mtsogoleri wampingowu ku Malawi Bishopu Brighton Vita Malasa ndi yemwe wanena izi mu kalata yomwe watulutsa mmalo mwa mpingowu mdzikomuno pomwe wati zomwe zachitikazi zikhonza kuchititsa kuti anthu aziopa kupita m’misonkhano yosiyanasiyana yokopa anthu.

Ambuye Malasa alimbikitsa ndikupempha anthu mdziko muno kuti ayesetse kuchita misonkhano yokopa anthu ya bata ndi mtendere poganizira kuti munthu wina aliyense ali ndi ufulu opita ku misonkhano ya ndale opanda mantha kuti akaphedwa kapena kuchitidwa chipongwe chilichonse.

Iwo apemphanso boma kuti likhwimitse chitetezo cha atsogoleri onse omwe azichititsa misonkhano yawo yokopa anthu powatumizira apolisi osungitsa bata kamba koti apolisiwa ali mdziko muno kuti ateteze anthu onse posatengera chipani chomwe ali.

Motsindika mpingowu wapempha atsogoleri andale kuti awonesetse kuti misonkhano yawo ikuchitika mopanda zipolowe komanso kuti achinyamata asamagwiritsidwe ntchito m’misonkhano kuti aziyambitsa ziwawa kamba koti uku ndikupha tsogolo la Malawi.

”Tikupempha a Malawi kuti asalole atsogoleri andale kutigawanitsa kudzera mukusiyana kwa zipani. Ziwawa ndichiopsezo chachikulu pa ulamuliro wa demokalase omwe ife eni ake tinsankha mchaka cha 1993 kudzera muchisankho chija cha liferendamu”chatero chikalatacho.

Chikalatachi chapitiriza ndikupempha anthu mdziko muno kuti asunge mtendere omwe dziko lino lili nawo kamba koti mtendere ndi chinthu chovuta kubwezeretsa.

”Sizisowa nthawi yochuluka kusokoneza mtendere wa dziko koma zimatenga zaka zochuluka kuti mtendere umangidwenso mdziko,”watero mpingowu.

Posachedwapa bungwe la mpingo wakatolika loona za chilungamo ndi mtendere CCJP linatulutsanso chikalata chopempha atsogoleri azipani kuti awonetse kuti m’misonkhano yawo mulibe ziwawa komanso linapempha bungwe loona zachisankho la MEC kuti lizalange atsogoleri omwe misonkhano yawo izakhuzidwe ndi ziwawa kuphatikizapo kuwachotsa kumene kuti asatenge nawo mbali pa zisankho.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>