Maphunziro a msukulu za masimba ati akuthandiza kuti ana azikhala otanganidwa ndi kuphunzira kuwerenga komanso kulemba.
Mlangizi wa zamaphunziro mu zone ya St. Anthony Thondwe m’boma la Zomba, mayi Mphatso Makhumula Namathawa ndi omwe anena izi pa mwambo wolandira aphunzitsi ongozipereka a msukulu za masimba mu zoni-yo. Iwo ati aphunzitsiwa akugwira ntchito yotamandika ndipo akuyenera kuyamikidwa pa ntchitoyi. Mutu wa tsikuli unali “Kugwira Ntchito Limodzi, Kuthandiza Ana Kuti Adziwe Kulemba Ndi Kuwerenga.”
Polankhulapo, Group Village Headman Chikapa ya kwa mfumu yaikulu Chikowi m’bomalo, yati ilimbikitsa makolo kuti azitumiza ana awo ku sukuluzi ndi cholinga choti adziwe kulemba ndi kuwerenga.