Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Fransiscoanakomana ndi mtsogoleri wa dziko la Palestine ku Vatican pa ulendo wake wokakomana ndi nduna yaikulu ya mdziko la Italy.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, a Mohmoud Abbas omwe ndi mtsogoleri wa dziko la Palestine achita izi pofuna kulandira madalitso apadera kuchokera kwa mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu ndi cholinga choti zokambirana zawo ndi nduna ya mdziko la Italy zikhale zabwino ndizothandiza kumanga ubale wabwino wa maiko awiriwa.
Mwa zina Papa wapempherera dziko la Palestine kuti mupitilire kukhala mtendere komanso chikondi.