Gulu la za uchifwamba la Taliban ati latulutsa kanema amene akuwonetsa amuna awiri omwe zigawengazi zinawaba ndipo zikuwasunga mokakamiza.
Malipoti a wailesi ya BBC ati Kelvin King wa mdziko la America komanso timothy Weeks wa mdziko la Australia anali aphunzitsi pa sukulu ya ukachenjede ya Afghanstan mu mzinda wa Kabul.
Amunawa ati anagwidwa ali mgalimoto mwawo panja pa sukuluyi m’mwezi wa august chaka chatha ndi anthu ena omwe anavala uniform ya achitetezo a dzikolo.
Malipoti ati izi zitachitika akuluakulu a chitetezo mdzikolo anayesetsa kuti apulumutse anthuwa koma zinakanika.
Kanema yomwe zigawengazi zatulutsa yomwe akuti yajambulidwa pa 1 mwezi uno ikufotokoza kuti anthuwa akusungidwa malo abwino koma apempha mtsogoleri watsopano wa dziko la America Donald Trump kuti apereke mkaidi m’modzi kuti anthuwa atuluke ndipo achenjeza kuti ngati savomera anthuwa aphedwa.