Mnyamata wina wa zaka khumi ndi zinayi (14) wafa atagwera mu mtsinje wina m’boma la Mangochi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo, Inspector Rodrick Maida, wati m’mawa wa lero pa 4 January 2018, mnyamatayu Adam Mdala anakwera njinga pochokera ku chigayo komwe makolo ake anamutuma ndipo atafika pa bridge ya mtsinje wa Lilasi, kaamba koti analephera kuwongolera bwino njingayo yomwe inawonongekanso ma brake anaphonya nsewu ndi kugwera mu mtsinjewo.
Anthu anamutengera ku chipatala cha Katuli komwe anatsimikiza kuti mnyamatayo wafa kaamba kobanika ndi madzi mu mtsinjemo.
Padakali pano apolisi m’bomali apempha makolo kuti aziwonetsetsa kuti njinga zawo ndi zoyenera kuyenda pa nsewu asanawapatse ana kuti ayendetse kuti apewe ngozi za mtunduwu.
Adam amachokera m’mudzi mwa Mpwakata kwa mfumu yaikulu Katuli m’boma lomwelo laMangochi.