Nduna ya zophunzitsa anthu, chikhalidwe ndi chitukuko cha ku midzi, mayiGrace Chiumiayawonjezera ndalama za mu ligi ya mpira wa miyendo yomwe imadziwika ndi kuti Obama Football League, yomwe anakhadzikitsa ku dera lomwe amayimira la Nkhata-BayWest Constituencykuchoka pa 1 Millionkufika pa 2.5 Million Kwacha.
Polankhula ndi atolankhani a Malawi News Agency(MANA) a Chiumia ati achita izi pofuna kuthandiza pachitukuko cha za masewero pakati pa achimamata a m’dera lawo.
Iwo ati mwa zina alinso ndi maganizo ofuna kukhadzikitsa timu ya mpira wa miyendo yomwe izidziwika ndi dzina loti Obama United.