Mipingo ya chikhristu yopezeka m’dera la aSenior Chief Chimwalam’boma laMangochiayiyamikira kamba kodzipeleka pa ntchito zolimbikitsa umodzi pakati pawo.
Mkulu woyendetsa ntchito za umodzi wa mipingo ya chi khristu mdelari bambo Dr. Joseph Kimu ndi omwe alankhula izi pa mwambo wa mapemphero a umodzi wa mipingoyi umene wachitika lero ku malo a parish ya mpingo wakatolika ya Kausi m’bomalo.
Iwo ati ndi okondwa kuona kuti mipingo yambiri yayamba kuonetsa chidwi chokhala nawo pa umodzi wa akhristu opezeka m’delari kusiyanana ndi pomwe bungwe loyimilira mipingo-yi limayamba m’delaro.
Polankhulanso wapampando wa bungwe loyimira mipingoyi aRaphael Sitima Banda a mpingo wa CCAP, nawo anayamikira mpingo wakatolika kamba kolimbikitsa umodzi wa mipingo ya chikhristu m’delaro.
Mipingo ya chikhristu yomwe inafika ku mwambo wa mapemphero a umodzi wa akhristu mdera la a Senior Chief Chimwala m’boma la Mangochi chaka chino inalipo 13 ndipo mipingoyi ndi monga wa Katolika,CCAP,Anglican, Churches Of Christ, Mboni Za Yesu, Providence Industrial Mission, Baptist, Evangelical Baptist, Assemblies Of God, Living Waters, Christian Church, Christian Pentecost, Topian komanso Abraham.