Bungwe lowona za kalembera mdziko muno la National Registration Bureau (NRB) lalengeza kuyambiranso kwa ntchito yolemba anthu mu kaundula wauzika mdziko muno.
Wofalitsa nkhani ku bungweli a Norman Fulatiraauza Radio Maria Malawi kuti ntchitoyi iyambiranso m’maboma onse a m’dziko lino ndipo ati izi zichitikira ku ma ofesi a bwanamkubwa m’boma lililonse.
Fulatira watsindikanso kuti kulembetsa koyamba mu ndondomekoyi ndi kwaulele ndipo wapempha onse omwe sanalembetse kuti akalembetse pa nthawiyi.