Mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse, Papa Francisco wati ndi wokhudzidwa ndi imfa ya anthu omwe afa pangozi ya moto umene unabuka pa chipatala cha Sejong m’dziko la South Korea.
Papa, wati zomwe zachitikazi ndi zokhudza kwambiri, ndipo wati ayikiza m’mapemphero, mizimu ya anthu-wa, ndi onse omwe akhudzidwa pa ngozi-yi.
Malingana ndi malipoti, anthu 37 ndi omwe afa pa ngoziyi.
Malipoti a Vatican News asonyeza kuti anthu ambiri mwa anthu omwe anamwalira ndi kuvulala pa ngoziyi ndi odwala omwe amalandira thandizo la matenda awo pa chipatalachi.