Ofesi yoona za mabungwe a utumuki wa a papa ku likulu la mpingo wakatolika m’dziko muno ya Ponfitical Mission Societies(PMS) yayamikira chidwi chomwe akhristu a mpingowu anaonetsa pothandiza kuti chaka utumiki wa ana cha Epifania chiyende bwino.
Mkulu wa ku ofesi-yi, ku likulu la mpingo-wu m’dziko muno , bambo Vincent Mwakhwawa, ndi yemwe wanena izi pofotokozera Radio Maria Malawi, za momwe chaka-chi chinayendera m’dziko muno.
Bambo Mwakhwawa ati chaka cha Epifania chomwe mpingo-wu unachita chaka chino, chinayenda bwino.
Polankhulanso mkulu wowona za mabungwe-wa mu dayosizi ya Mzuzu, bambo Phillip Shawaathokozanso a ku likulu la ofesiyi ku ECM,kamba ka chidwi chomwe anaonetsa pothandizanso ma dayosizi kuti akonzekere bwino chakachi, zomwe zathandiziranso kuti chakachi chikhale chopambana.