Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo wa CCAP Upemphelera Mvula

$
0
0

Mpingo wa CCAP mu Sinodi ya Blantyre wachita mapemphero apadera, opempha mulungu, kuti adalitse dziko lino ndikulipatsa mvula yabwino.

M’modzi mwa akulu-akulu mu mpingo-wu, m’busa Alex Maulana, wati mpingo wa CCAP mu Sinodi-yi wachita mwambowu kaamba kokhudzidwa ndi malipoti akusowa kwa mvula m’madera ochuluka m’dziko muno.

Iwo ati ngati zinthu zitapitilira kukhala chomwechi ndiye kuti dziko lino litha kukomananso ndi mavuto a njala zomwe zingasokoneze miyoyo ya anthu mdziko muno.

Iwo ati akukhulupilira kuti mapephero omwe mpingowu wachita abala zipatso zabwino komanso kuti mulungu ayankha mapempherowa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875