Makwaya a mu mpingo wakatolika ati akuyenera kuzindikira kuti akuyenera kuyika chikhristu patsogolo pogwira ntchito zawo mu mpingo.
Bambo Lawrence Kudzingo otumikira mu dayosizi ya Dedza ndi omwe alankhula izi lero pambuyo pa m’bindikiro wa masiku awiri wa kwaya ya St. Pius ya ku parishi ya Ntcheu mu dayosiziyo inali nawo.
Iwo ati zimakhala zomvetsa chisoni pamene nthawi yao ya utsogoleri watha kapena kuyimitsidwa kumene, amasiya kutenga nawo gawo mu zochitika za mu mpingo.
Polankhulapo wapampando wa kwaya ya St Pius a Lighton Thumba ati apindula ndi m’bindikirowu kaamba koti azindikira zomwe mkhristu akuyenera kuchita posatengera magawo omwe akutumikira mu mpingo.