Sisiteri wa m’dziko la Colombia yemwe akusungidwa mokakamiza ndi zigawenga za Al-Qaeda mdziko la Mali, wapempha mtsogoleri wa mpingo wakatolika padziko lonse Papa Francisco kuti athandize pa ntchito yokambirana ndi zigawengazo kuti zimutulutse.
Sisiteriyo, Grolia Cecilia Argoti wa zaka 57 zakubadwa wakhala akutumikira mdziko la Mali kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anagwidwa ndi kuyamba kusungidwa mokakamizidwa ndi zigawengazo m’mwezi wa August 2017.
Uthenga wa mphindi zoposa zinayi omwe zigawengazi zatumiza, anthu amva Sister Argotiakupereka pempholi kwa Papa Francisco.
Malipoti akusonyeza kuti zigawengazo zikusunga sisiteriyo pofuna ndalama kuti apulumutsidwe.