Bwalo la Chief Resident Magistrate m’boma la Zomba, likuyembekezeka pa 8 mwezi uno kuzapitirira kumva mlandu wa nduna ya kale ya zamalimidwe a George Chaponda omwe akuwazenga mlandu powaganizira kuti anagula chimanga mwachinyengo mdziko la Zambia.
Bwaloli lakana pempho la mbali yoyimbidwa mlandu kuti mlandu wa a Chaponda ndi a Rashid Tayub omwe akuyimbidwa mlandu wopeza mwachinyengo contract yonyamula chimanga uyimbidwe mosiyana kaamba koti ati zichedwetsa mlanduwu.
Patsikuli bwaloli lakananso pempho la mbali ya boma loti mboni zomwe zinaperekera kale umboni mu bwaloli ziperekenso umboniwo ponena kuti ma umboni onse anamveka bwino lomwe ndipo palibe chifukwa chobweretseranso mbonizi.