Ophunzira a mpingo wa katolika msukulu za sekondale mdziko muno awapempha kuti akhale owonetsa makhalidwe abwino.
Mkulu wa ku ofesi yoona za utumiki wa apapa ya Pontifical Missionary Societies (PMS) ku likulu la mpingo wa katolika mdziko muno ku Episcopal Conference of Malawi (ECM) bambo Vincent Mwakhwawa anena izi pambuyo pa msonkhano wa masiku awiri wa bungwe la ophunzira achikatolika msukulu za sekondale la Young Christian Students (YCS) omwe unachitikira ku Our Lady of Africa mu arkidayosizi ya Lilongwe.
Iwo ati ophunzirawa akuyenera kukhala akhristu olimba popereka uthenga wabwino wa yesu khristu kwa anzawo ndi kutsata komanso kuwonetsa moyo wa chikatolika paliponse pomwe akhala.
Apempha Akhristu Azipemphelera a Sisteri
Mkulu wa asisteri a chipani cha Franciscan ku parishi ya St. Dennis mu arkidayosizi ya Lilongwe sister Sabina Mwamba wapempha akhristu kuti azipemphelera asisteri mdziko muno.
Sister Mwamba anena izi pa mwambo wa nsembe ya ukaristia yomwe inachitikira ku mphakati wa St. Matias mu parishiyi, pomwe sister Mercy Ndalama omwe ndi membala wa mphakati-wu amakondwelera kuti achita malumbiro awo oyamba a usisteri mchipanichi.
Pamwambowu sister Mwamba alengeza kuti sister Ndalama ayamba kugwira ntchito yawo yophunzitsa, yothandiza ana a masiye komanso yothandiza anthu odwala mzipatala mdziko la Zambia.