Pafupifupi anthu mazana asanu ndi limodzi (600), ali pakawuniwuni wa matenda a Ebola m’dziko la Mali.
Anthuwo akuwunikidwa ndi azaumoyo pamene dzikolo likupitiliza kuyesetsa kuti matendawa omwe apha kale anthu anai m’dzikolo asapitilire kufala. Anthuwo akuwunikidwa powakaikira kuti agwidwa ndi matendawa pomwenso akuluakulu a boma anakumana pofuna kupeza njira zokhwimitsira chitetezo mmalire a dzikolo ndi maiko ena. Malipoti a BBC asonyeza kuti anthu awiri ndi omwe awapeza ndi matendawa .