Chisankho cha pulezidenti chapadera mdziko la Zambia chichitika pa 20 January chaka cha mawa pofuna kupeza mtsogoleri yemwe alowe mmalo mwa mtsogoleri wakale wa dzikolo malemu Micheal Sata.
Mtsogoleri wogwirizira Guy Scott, yemwe malamulo adzikolo sakulola kuti adzapikisane nawo paudindowu, kamba koti makolo ake sanali nzika za dzikolo.
Iye walengeza izi lachiwiri ndipo wapempha atsogoleri a ndale mdzikolo kuti asunge bata ndi mtendere.
Padakali pano mchipani cholamula cha Patriotic Front muli kusamvana kamba koti Pulezidenti Scott anachotsa mlembi wamkulu wachipanicho pa 3 November popanda chifukwa chenicheni.
Pulezidenti wa dzikolo Michael Sata anamwalira lachiwiri pa 28 October pa chipatala cha King Edward 7 mumzinda wa London ndipo anaikidwa mmanda lachiwiri pa 11 mwezi uno.