Nyumba zofalitsa nkhani m`dziko muno azipempha kuti zizilemba nkhani zoona zokhazokha zokhudza matenda a EDZI.
Mkulu wogwilizira udindo woona za mapologalamu ku bungwe la National Aids Commission (NAC) Dr Andrina Mwansambo ndi amene anena izi lachiwiri mu mzinda wa Lilongwe.
Dr Mwansambo ati bungwe lawo liwonetsetsa kuti nyumba zofalitsa nkhani zizipereka mauthenga oyenera okhudza matenda a Edzi kamba ka zomwe anthu ena akunena kuti mankhwala a matendawa apezeka.
Iwo apempha atolankhani kuti afufuze bwino kuti anthu asakhale ndi maganizo olakwika okhudza nkhaniyi.
Mayi Mwansambo ati padakali pano palibe makhwala ochizira matendawa koma mankhwala amene alipo ndi otalikitsa moyo chabe otchedwa Antiretrovial ARV.
Malinga ndi malipoti a bungwe loona za matenda a Edzi pa dziko lonse, mu chaka cha 2013,anthu 10 aliwonse pa anthu 100 anali ndi matenda a Edzi mdziko la Malawi.