Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chipani cha Patriotic Front Chayimika Pulezidenti Scott Kukhala Membala wa Chipanichi

$
0
0

Chipani cholamula mdziko la Zambia  cha Patriotic Front  chayimika Pulezidenti wadzikolo  Guy Scott kukhala membala wachipanicho kwa miyezi iwiri.

Chipanicho chayimika Pulezidenti Scott yemwe akugwirizira udindowu kamba kochita zinthu mosatsata malamulo.

Zinthu sizikuyenda bwino kwenikweni mchipanicho pamene anthu akuyembekezeka kusankha mtsogoleri yemwe alowe mmalo mwa Pulezidenti Michael Sata, yemwe anamwalira pa 28 October chaka chino ali pa udindowu.

China mwa Zifukwa chomwe Pulezidenti Scott akudzudzulidwa nacho ndi kukakamiza atolankhani maka a nyumba  zofalitsa nkhani za boma kulemba nkhani zabwino zokhudza iye yekha.

Chisankho chapadera mdzikolo chichitika pa 20 January chaka cha mawa ndipo Pulezidenti Scott sadzayima nawo kamba koti si nzika ya dzikolo.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>