Akhristu a ku St Cecilia ku St James Catholic Parish ku Chilomoni a mpingo wakatolika mu Akidayosizi ya Blantyre awayamikira kamba kochitapo kathu pomanga tchalitchi lawo modzidalira.
A Vicar General mu Akidayosiziyo Monsinyo Bonface Tamani amalankhula izi lamulungu pa mwambo wotsekulira ndi kudalitsa tchalitchili.
Monsinyo Tamani ati zomwe akhristuwa achita zasonyezadi poyera kuti ayamba kudziwa za udindo wawo wodzipereka pogwira ntchito zotukula mpingowu.
Iwo anati,“Ine ndili wokondwa kuona tchalitchi chimene akhristu amanga kamba koti kukhala ndi tchalitchi ndi chinthu chabwino ndipo anthu amapita kukatolako nzeru za Mulungu.”
Pamenepa Monsinyo Tamani alimbikitsa akhristuwo kuti apitilize kukhala ndi mtima wopereka monga asonyezera pomanga tchalitchilo komanso owopa Mulungu.
Tchalitchi chatsopanochi ndi imodzi mwa nthambi za parish ya St James Chilomoni mu Arkdiocese yo.