Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Olumala Akusowa Zipangizo Zamakono Zogwiritsa Ntchito

$
0
0

Bungwe lowona za ufulu wa anthu olumala la Federation of Disability Organisation in Malawi FEDOMA ladandaula chifukwa cha kusowa kwa zipangizo za makono zomwe anthu olumala angamagwiritse ntchito.

Mkulu wa bungweli Action Amosi ndiye walankhula izi pa msonkhano wa olemba nkhani omwe bungweli linachititsa mu mzinda wa Blantyre.

Bungwe la Fedoma likuyankhula izi pamene likukonzekera mwambo wokumbukira anthu olumala pa dziko lonse lapansi womwe udzachitike pa 13 mwezi uno mu mzinda wa Lilongwe.

Iwo ati bungwe lawo ndi lokhumudwa kamba koti lamulo lomwe linakhazikitsidwa ndi boma mu chaka cha 2012 lokhudza anthu olumala sakupindula nalo.

A Amosi ati, “tsiku limeneli ndi limene timayang’ana mmbuyo kuti ngati anthu olumala mu chaka chapitachi tapindula bwanji.”

Polankhulapo wachiwiri kwa mkulu wowona za anthu olumala mu nthambi yowona zoti palibe kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ndi chisamaliro cha anthu olumala a Felix Sapala ati boma likuwonetsetsa kuti nthambi zonse za boma zikupanga malamulo komanso kupereka mwayi kwa anthu.

“Malamulo a dziko lino amapereka mphamvu zakuti ma unduna atumikire anthu moyenera malinga ndi ntchito zomwe undunawo umagwira,” anatero a Sapala.

Iwo ati boma liwonetsetsa kuti lamulo  lakuti zipangizo zamakono zikamapangidwa zizikhala zakuti anthu olumala atha kugwiritsa ntchito, likugwira ntchito.

Padakali pano dziko la Malawi lili ndi chiwerengero cha anthu olumala choposera 6 hundred thousand omwe ambiri amakhala mmadera a ku midzi ndipo amakumana ndi mavuto osiyanasiyana.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>