Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Nkhanza za kwa Ana Zikusokoneza Maphunziro

$
0
0

Ana ambiri akuti akulephera kuchita bwino pa maphunziro awo kamba ka nkhaza zomwe amakumana nazo pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Mkulu woona za chitetezo cha ana ku bungwe la Plan International Malawi Link a Grant Kadzulungo ndiwo anena izi lachisanu m`boma la Mangochi pomwe bungweli  limafotokozera khonsolo ya boma la Mangochi za pulojekiti yomwe bungwei likuyembekezeka kukhazikitsa m`bomali yotchedwa Learn Without Fear.

Iwo ati ana amakumana ndi khaza zambiri m`moyo wawo  koma amalephera  kuti abwere poyera kamba ka mantha.

A Kadzulungo ati ayika mabokosi a chinsinsi mmasukulu ndi cholinga choti ana azitha kufotokoza zomwe zimawasangalatsa  komanso zoyipa zomwe zikuwachitikira pa moyo wawo.

“Pulojekitiyi ithandiza ana kuti akhale odziyimira pawokha komanso kuti aziwulura zovuta zomwe amakumana nazo,” anatero a Kadzulungo.

Iwo ati ntchitoyi ikufuna kuwonetsetsa kuti mavuto a kugwilira, komanso kugwiridwa ziwalo zobisika zitheretu kamba koti awa ndi ena mwa mavuto aakulu omwe akubwezeretsa mmbuyo maphunziro kwa atsikana.

Bungweli likuyembekezeka kugwira ntchitoyi kwa zaka ziwiri m’ma zone awiri a bomali momwe muli sukulu 32.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>