Archdayosizi ya Blantyre yayamikira ubale wabwino womwe ulipo pakati pa dayosiziyi ndi dayosizi ya Lichinga mdziko la Mozambique.
Arch Episkopi wa archdayosiziyo Ambuye Thomas Luke Msusa ndi omwe ayamikira ubale wamadayosizi awiriwa lamulungu pa 7 December pa chikondwerero cha nkhoswe ya parish ya St.Francis mu dayosizi ya Lichinga mdzikolo.
Iwo ati ubalewu si wa ma Episkopi okha komanso akhristu eni ake a mmadayosizi awiriwa.
Ambuye Msusa,omwenso anatsogolera mwambo wa misa mchilankhulo chachipwitikizi kwa nthawi yoyamba, ati ubale wa madayosizi awiriwa uthandiza kwambiri polimbikitsa moyo wa mapemphero,pamene akhristu a mmadayosizi awiriwa azikhala akuyenderana.
Ena mwa akhristu a mu archdayosizi ya Blantyre anali nawo pa mwambowo.