Mtsogoleri wadziko lino professor Arthur Peter Mutharika,wapempha a Malawi kuti apemphere kuti mvula iyambe kugwa.
Pulezidenti Mutharika wanena izi kudzera mchikalata chomwe nthambi yofalitsa nkhani kunyumba ya boma yatulutsa.
Iye wati ndi wokhudzidwa powona kuti mvula, sidayambe kugwa mmadera ambiri omwe pano amayenera kukhala atayamba kale kulandira mvula.
Pulezidenti Mutharika wapempha a Malawi onse kuti mathero a sabata ino kuyambira lachisanu mpaka mtsogolomu,akhale akupemphera mwapadera kuti Mulungu adalitse dziko lino ndi mvula yabwino yomwe ingathandize kuti mdziko muno mukhale chakudya chokwanira.
Mutharika wapemphanso magulu osiyanasiyana omwe amachita mapemphero maka nthawi ya nkhomaliro tsiku lililonse mmizinda komanso mmatawuni,kuti apemphererenso mvula mkatikati mwa mapemphero awo.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wapempha nduna za boma,aphungu akunyumba yamalamulo komanso akuluakulu onse a mmabungwe a boma ndinso omwe siaboma,kuti asalephere kukapemphera kumathero a sabata mmatchalitchi komanso mmizikiti yawo ngati njira imodzi yolimbikitsira mapempherowa.