Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Boma Latsutsa za Kusalabadira kwa a Mutharika ku Mavuto a Dziko Lino

$
0
0

Boma lati sizowona kuti mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika sakulabadira za mavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo omwe adza chifukwa cha mavuto a zachuma.

 

Boma lanena izi kudzera mchikalata chomwe latulutsa, chomwe chasayiniridwa ndi nduna yofalitsa nkhani, zokopa alendo ndi chikhalidwe cha anthu a Kondwani Nankhumwa

Chikalatacho chadzudzula mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress MCP Dr Lazarus Chakwera kamba kowuza mtundu wa a Malawi kuti Pulezidenti Mutharika sakusamala za mavuto omwe dziko lino likukumana nawo pamene boma lake likukweza malipiro a akuluakulu ogwira ntchito m’boma.

Kudzera mchikalatachi Pulezidenti Mutharika sagonjera anthu amene akuwoneka kuti ali ndi mayankho onse a mavuto omwe dziko lino likukumana nawo kamba koti iye akudziwa kuti iwo akuchita izi pa zifukwa za ndale.

Chikalatacho chati aliyense akuzindikira kuti a Mutharika mmene amatenga utsogoleri wa dziko lino ndalama za boma zinali zitasakazidwa ndipo mayiko amene amathandiza dziko lino anali atasiya.

Icho chati pozindikira izi Pulezidenti yu adakhazikitsa ndondomeko zosiyanasiyana pofuna kusamala chuma cha boma.

Boma latulutsa chikalatachi a Chakwera atauza msonkhano wa atolankhani lolemba mu mzinda wa Lilongwe kuti a Mutharika ndi mtsogoleri yemwe akuchita zosemphana ndi zomwe iye mwini adalonjeza mtundu wa a Malawi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>