Dayosizi ya Chikwawa yayamikira ntchito zomwe mabungwe a mu mpingo wa katolika akhala akugwira mchaka chomwe chikuthachi.
Mlembi wamkulu mu dayosiziyo Bambo Patrick Jambo,ndi omwe ayamikira mabungwewa lachiwiri pomwe Radio Maria Malawi imafuna kudziwa momwe dayosiziyo yagwilira ntchito zake mchakachi.
Iwo ati ndi wokhutira ndi momwe mabungwewa akhala akugwilira ntchito pothandiza kufalitsa uthenga wa mulungu kudzera mu ntchito zawo.
Bambo Jambo ati dayosizi ya Chikwawa, imakumana ndi mavuto ambiri monga kusefukira kwa madzi ndipo ayamikira bungwe lowona za chitukuko mu mpingowu la Cadecom komanso mabungwe ena a mu mpingowu chifukwa chodzipereka pothandiza kutukula miyoyo ya anthu.
Ku mbali ya maphunziro iwo ati sanathe kukwanilitsa zina zomwe amafuna koma ati akuyesetsa kuti maphunziro akhale akupita patsogolo maka ku sukulu zomwe za mpingo wakatolika mu dayosiziyo.