Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ana Awiri a Banja Limodzi Afa ndipo Ena Awiri Avulala Khoma la Nyumba Litawagwera

$
0
0

Ana awiri a banja limodzi afa ndipo ena awiri avulala khoma la nyumba yomwe anagona litagumuka ndikuwapsinja ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.

Anawo, Agness ndi Pemphero Chaona omwe amakhala ku Machinjiri area 6 akuti afera kunyumba kwa nzawo wina komwe amakacheza ndipo kutada anaganiza zongogona komweko.

Mneneli wa apolisi ku Blantyre, Sub Inspector Elizabeth Divala watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati ana ena awiri omwenso anali mchipindamo avulala pangoziyo.

Malinga ndi a Divala mvula yamphamvu yomwe inagwa usiku wa lachiwiri inachititsa kuti mpanda wa nyumba ina yoyandikana ndi nyumbayo unagwera khoma la chipinda chomwe anawo anagona zomwe zinachititsanso kuti khomalo ligwe ndi kupsinja ana anayi omwe anagona mchipindamo.

Iwo ati ana awiri Caroline wa zaka 10 ndi Tawina Ntipo wa zaka zitatu anavulalanso pa ngoziyo ndipo anawatengera ku chipatala chachikulu mu mzindawo cha Queen Elizabeth komwe anakalandira thandizo.

Padakali pano mwambo woyika mmanda matupi a Agness ndi Pemphero omwenso anali ana okhawo a mmbanja la Chawona uchitika lero lachinayi ku Manyowe mu mzinda womwewo wa Blantyre.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>