Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati kusiyana maganizo kwa ma episikopi pa nkhani zokhudza banja,sizikutanthauza kuti mu mpingowu muli kugawikana.
Papa Francisco amalankhula izi dzulo polankhula kwa anthu omwe amasonkhana kulikulu la mpingowu mwanthawi zonse ,kuti apemphere limodzi ndi Papa komanso kumva zomwe wawakonzera kuti adziwe.
Mtsogoleri wampingo wa katolikayu, wanena izi poyang’anira momwe nyumba zofalitsa nkhani zimawulutsira msonkhano wa ma episikopi owunika nkhani zokhudza banja omwe unachitika mmwezi wa October chaka chino.
Iye wati atolankhani ena amawulutsa nkhaniyi ngati akuwonera masewero a mpira omwe amakhala ndi mbali ziwiri.
Iye wati ndi zowona kuti panali kusiyana maganizo pankhaniyi, koma wati uwu unali mwayi wawukulu wakuti anthu adziwe za ufulu omwe uli mumpingowu pofuna kuthandiza anthu kuyanjana ndi Mulungu.