Kulimbikitsa maphunziro a atsikana ndi njira yabwino yomwe ingathandize dziko lino pothana ndi m’chitidwe wa nkhanza pakati pa amayi ndi atsikana.
M’modzi mwa aphungu omwe ali ndi luso la mayimbidwe ku nyumba ya malamulo olemekezeka a Lucius Banda ndi omwe anena izi pofotokozera mtolankhani wathu.
A Banda ati atsikana amene anachita bwino pa maphunziro awo amatha kuzitetedza okha ku nkhanza zosiyanasiyana zomwe amakhala akukomana nazo nthawi zonse.
Pamenepa a Banda apempha mabungwe omwe akugwira ntchito zolimbana ndi nkhanza pakati pa amayi ndi atsikana kuti azikonda kugwilitsa ntchito anthu aluso monga oyimba, alakutuli, ndi cholinga choti mauthenga okhudza nkhanza azitha kufikira anthu ambiri mdziko muno.
Iwo apempha mabungwe kuti afikile anthu onse mmadera a ku midzi a mdziko muno mziyankhulo zonse zomwe angagwiritse ntchito kuti apewe kuwononga ndalama zambiri.
A Banda ati atsikana akuyenera kuyika maphunziro patsogolo kuti apewe mavuto amene amadza kamba kosadziyimira pawokha.