Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ana Awiri Afa Atamira pa Dziwe la Madzi

$
0
0

Ana awiri a banja limodzi m’boma la Dowa afa atamira padziwe la madzi m’bomalo.

Ofalitsa nkhani za apolisi mbomalo  Sergent Richard  Kaponda watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati anawo anamwalira lachitatu atapita kudimba ndi amayi awo.

Iwo ati ali kudimbako anawo anapita padziwe lina lomwe linali pafupi komwe amakasambira. Ali mkati mosambira mmodzi mwa anawo anapita mbali yozama ya dziwelo ndipo mbale wakeyo anamutsatira pomwenso naye anamira.

A Kaponda ati amuna ena omwe analowa mmadzimo ndi omwe anapeza matupi a anawo atakakamira mmatope ndipo anawachotsa.

Malipoti achipatala asonyeza kuti anawo anamwalira kamba koti amalephera kupuma.

Anawo omwe ndi Blessings Kamwaza wa zaka 11 zakubadwa komanso Chrissy Kamwaza 10 ankachokera mmudzi mwa a Kamkwamba kwa mfumu yayikulu Mkukula m’boma lomwelo la Dowa.

Ngoziyi yachitika pamenenso ana ena awiri mu mzinda wa Blantyre ayikidwa mmanda khoma la nyumba litagwera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>