Maepisikopi a mdziko la America adzudzula apolisi ku mchitidwe omawopseza anthu oganiziridwa milandu omwe akuti wakula kwambiri mdzikolo.
Ma episikopiwa adzudzula apolisiwo zitamveka kuti iwo akumagwiritsa ntchito njira zosavomerezeka zomwe ndikuphatikizapo kuwopseza, akafuna kupeza umboni pankhani zomwe anthu akuganiziridwa.
Iwo ati uku nkulakwa kwakukulu kamba koti anthuwo, amakhala ndi ufulu wachibadwidwe olandira chilungamo.
Iwo ati mpingo wakatolika, sumagwirizana ndi mchitidwe otere,ndipo ati palibe mfundo zomwe apolisi anganene kuti adzichita nkhanza zotere kwa anthu oganiziridwa milandu.