Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la CRECCOM Liyamikira Mafumu Mboma a Mangochi

$
0
0

Bungwe la CRECCOM layamikira gawo lomwe mafumu akutenga m’boma la Mangochi polimbikitsa maphunziro a asungwana.

Mkulu wa bungweli mayi Ziwone Mussa ndi yemwe wanena izi pamwambo opereka mphatso kwa asungwana omwe achita bwino kwambiri mchigawo choyamba chamaphunziro chomwe chatha sabata yapitayi. Mai Mussa ati bungwe lawo lakhutira ndi gawo lomwe mafumu m’boma la Mangochi akutenga polimbikitsa maphunziro a asungwana, poyerekeza ndi momwe zikukhalira m’maboma ena momwe bungweli likugwiramo ntchito zake.

Mayi Mussa  mwapadera ayamikira mfumu yaikulu Chowe, chifukwa choika malamulo apadera omwe akuthandiza kuti asungwana asasiyire sukulu panjira, komanso kuti omwe adasiya pazifukwa zosiyanasiyana abwelere ku sukulu

 “Tikungwira ntchito m’maboma anayi Chikwawa Thyolo, Nsanje ndi Mangochi, pa maboma anayi amenewa Boma la Mangochi ndi lomwe lachita bwino, maka chifukwa mafumu akutenga nawo gawo polimbikitsa atsikana kupita ku sukulu.”anatelo mayi Mussa”.

  Pamwambowo asungwana omwe achita bwino mchigawo cha maphunziro chomwe changothachi kuphatikizapo omwe ayambanso sukulu atasiya,alandira mphatso zosiyanasiyana monga zikwama ndi zina zotelo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>