Arkdayosizi ya Blantyre yapempha anthu akufuna kwabwino kuti athandize arkdayosiziyi pobweza ngongole yomwe kampani yake yotsindikiza mabuku ya Montfort Press ili nayo.
Arkidayosiziyi yapereka pempholi pamene ikupitiliza kutsata njira zosiyanasiyana pofuna kupeza ndalama zobwezera ngongoleyi,yomwe yatsala pafupifupi 40 miliyoni kwacha.
Mlembi wa arkepiskopi mu arkdayosiziyo Bambo Michael Chimwala,wawuza mtolankhani wathu, kuti mundondomeko yofuna kupeza zina mwa ndalamazi yomwe arkdayosiziyi inakonza pa 5 December, inapeza ndalama zopitilira zomwe imayembekezera,zomwe zikupereka chilimbikitso choti kubweza ngongoleyi ndi thandizo la akhrisitu eni ake komanso onse akufuna kwabwino,ndi kotheka.