Nthambi yowona za matenda a Edzi mu unduna wa za umoyo yati anthu khumi ndi asanu 15 mwa anthu 100 aliwonse mdziko muno akumasiyira panjira kumwa mankhwala otalikitsa moyo a ARV pa zifukwa zosiyanasiyana.
Mkulu owona za matenda a Edzi mu nthambiyi Dr.Frank Chimbwandira ndi omwe anena izi lachinayi m’boma la Mangochi, pomwe bungwe la St.Egidio,kudzera mu project yake ya DREAM,limamva malipoti ochokera mzipatala zomwe zimagwira ntchito limodzi ndi bungweli pankhani zokhudza matenda a Edzi.
Dr Chimbwandira,ati padakali pano dziko lino lili ndi anthu oposa 500 sauzande omwe amalandira mankhwala otalikitsa moyo,koma 15 mwa anthu 100 aliwonse pakati pa anthuwa akumasiyira panjira kumwa mankhwalawa pa zifukwa zosiyanasiyana.
Iwo atinso ntchito yofufuza ana omwe abadwa ndi kachirombo ka matendawa yotchedwa Early Infant Diagnosis E.I.D, ikukumananso ndi mavuto aakulu maka a mayendedwe kuti magazi omwe akutengedwa mzipatala azikafika mzipatala zomwe zili ndi makina oyezera magaziwa.