Bungwe la Civil Liberties Committee (CILIC),lapempha anthu akufuna kwabwino kuti adzipereke pothandiza anthu osowa panthawi ino ya chikondwerero cha Khirisimasi ndi chaka chatsopano.
Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli Mayi Emmie Chanika apereka pempholi pomwe bungweli limapereka thandizo losiyanasiyana ku chipatala cha Queen Elizabeth Central komanso ku ndende ya Chichiri mu mzinda wa Blantyre.
Mayi Chanika ayamikira mabungwe omwe ayamba kale kuyendera anthu omwe ali kundende komanso mzipatala, pofuna kugawana nawo mphatso zomwe ali nazo.
Iwo ati panthawiyi anthu akumbukirenso kuthandiza ana komanso okalamba amene akusowa thandizo losiyanasiyana pa moyo wawo, kuti chikondwerero cha Khirisimasi chikhale chopambana kwa aliyense.
Wina mwa katundu yemwe bungwe la CILIC lapereka ku ndende ya Chichiri komanso chipatala cha Queens ndi zovala,zofunda komanso nsapato zomwe bungweli lalandira kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino kuti lithandizire anthu osowa.