Diocese ya Zomba ayiyamikira chifukwa chotenga gawo lalikulu lothandiza kupititsa patsogolo ntchito zokweza umoyo wa ana mu Diocese-yo.
Mfumu yayikulu Mlumbe ya m’boma la Zomba ndi imene yanena izi itakhala nawo pa mwambo wa tsiku loganizira za umoyo wa ana umene Diocese-yo inachititsa sabata yapitayi.
Mfumuyi yati ndiyokhutira kwambiri ndi momwe mpingo wakatolika ukudziperekera pantchito za umoyo m’bomalo.
Iwo apempha mafumu m’bomalo kuti achepetse mchitidwe ophwanya ufulu wa ana ndipo alimbikitsa mafumu kuti atengepo gawo lalikulu pokweza ntchito za umoyo.
Polankhulapo mkulu wa bungwe la Catholic Health Commission mu Diocese-yoMayiGrace Makonyolaanati bungwe lawo linawona kuti ndi chinthu cha mtengo wapatali kuti chakachi chisanathe lisonkhanitse mabungwe ndi anthu a mu Diocese-yo pamodzi.
Cholinga cha msonkhanowo chinali kufalitsa uthenga wakuti mwana aliyense ali ndi ufulu wolandira chithandizo cha za umoyo kuti akule ndi moyo wabwino kutinso adzakhale nzika yabwino ya dziko lino la Malawi.