Wachiwiri kwa mkulu wowona za ma programme ku Radio Maria Malawi Bambo Charles Kaponya, wati wailesiyi ichita chotheka kukonza mavuto omwe ma studio ang’onoang’ono a wailesiyi akukumana nawo mdziko muno.
Bambo Kaponya, amalankhula izi Loweruka, pomwe amakumana ndi mavolontiya a ku studio ya Zomba komanso abwenzi a mudayosiziyo, pofuna kudziwana nawo,pomwe angoyamba kumene kutumikira paudindowu.
Iwo ati amvetsa kuti ntchito yotumikira Mulungu kudzera ku Radio Maria mmastudiowa,ikukhala yovutirapo chifukwa cha mavuto osiyanasiyana, ndipo ati wailesiyi iyesetsa kukonza ena mwa mavutowa.
Bambo Kaponya alimbikitsa ma volontiya onse kuti apitirize ntchito yopambana yomwe iwo akugwira, ndipo kuti mavuto amene akukumana nawo asawabwezeretse m’mbuyo pa utumiki wawo.
Mkulu wa studio ya Zomba mayi Elizabeth Mitha ati mkumanowu uthandiza kwambiri kamba koti ali ndi chiyembekezo kuti akuluakulu a ku wailesiyi achitapo kanthu pa mavuto amene akukumana nawo.