Episkopi wa dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Sitima,wapempha mamembala a bungwe la amayi mu mpingowu kuti akwaniritse mfundo zomwe amanga kumsonkhano wawo waukulu, womwe watha lamulungu ku sukulu ya sekondale ya atsikana ya Mary Mount mu dayosizi ya Mzuzu.
Polankhula pambuyo pa nsembe ya misa yotsekera msonkhanowu, Ambuye Sitima alangiza amayiwa, kuti pasathe mwezi asadagawire anzawo mfundo zomwe atenga kumsonkhanowu komanso kuti akwaniritse mfundozi akafika mmadayosizi awo.
Zina mwa mfundo zomwe awunikirana ku msonkhanowu ndi kuti amayi asakhale a mantha potumikira Mulungu ndi powunikira zinthu zomwe zikulakwika mu mpingo ngakhalenso mdziko.
Ku msonkhanowu amayiwa agwirizana kuti azikhala okondana, okhulupirirana, achiyanjano monga ulili Utatu Woyera ndiponso kukhala odekha monga mmene analili amayi Maria.
Amayiwa akambirananso kuti mavuto amene amakumana nawo pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku asalekanitse ubale wawo ndi Mulungu.
Msonkhanowu womwe ndi wanambala 36, unayamba Lachitatu pa 17 mwezi uno ndipo watha lamulungu pa 21,pamene amayi a m’bungweli ochokera mmadayosizi onse asanu ndi atatu a mpingowu anakumana.