Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mafumu a M’boma la Ntcheu Ayamikira Bungwe la CCJP

$
0
0

Mafumu m’boma la Ntcheu ayamikira ntchito yokhudza Chilungamo Choyambilira yomwe nthambi yowona za Chilungamo ndi Mtendere mu mpingo wakatolika mu arkidayosizi ya Lilongwe, imagwira m’bomalo ndi thandizo lochokera ku International Development Fund.

Polankhula  ndi Malawi News Agency lachiwiri,mfumu yayikulu Kwataine ya m’bomalo yati maphunziro okhudza chilungamo choyambilira chomwe magulu oweruza milandu akumidzi alandira kuchokera ku bungweli, athandiza pochepetsa chinyengo komanso kukondera pakaweruzidwe ka milandu mmidzi ya mafumu.

Mfumu Kwataine yati pulojekiti ya Chilungamo Choyambilira yathandizanso kuchepetsa mavuto omwe anthu amakumana nawo akafuna kupeza chilungamo kamba koti zimakhala zovutirapo kuti achoke mmidzi yawo kuti akafike ku polisi komanso ku mabwalo amilandu.

Padakali pano pulojekiti ya Chilungamo Choyambilira,yakhazikitsanso mabuku osungiramo nkhani zokhudza milandu mmudzi uliwonse mdera la mfumu Kwataine ndi cholinga choti azisungiramo mbiri ya milandu yomwe  yafika mmagulu oweruza milanduyo,zomwe akuti  zithandiza kukumbukira zigamulo zomwe zidaperekedwa kale milandu ikakhala yofanana.

Pothilirapo ndemanga, mkulu owona za mapulogalamu  okhudza chilungamo choyambilira m’bomalo a Mike Makalande, ati ndi okondwa powona kuti anthu mdera lomwe bungwe la CCJP limagwiramo nthitoyi, ayamba kuzindikira komwe angakapeze chilungamo choyambilira monga kwa  apolisi akumidzi komanso makhothi a mmidzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>