Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la PMS Layamikira Makolo ndi Atsogoleri a Mpingo Pokometsa Utumiki wa Ana

$
0
0

Mkulu woyan’ganira mabungwe a utumiki wa a Papa m’dziko muno,  wayamikira makolo ndi atsogoleri a mpingo  chifukwa chothandiza kukometsa chaka cha  utumiki wa ana  chomwe chachitika  lamulungu la Epifania.

Bambo Vincent Mwakhwawa alankhula izi pa mwambo wa nsembe ya misa yomwe akhristu a ku parish ya St Martin de Porresku Dedza anali nayo, yomwenso zochitika zambiri pa misayi zinatsogoleledwa ndi ana.

Bambo Mwakhwawa ati mpingo wakatolika ndi wokondwa kuti chaka chino ana anapatsidwa mpata wokwanira wotha kutumikira Mulungu mmatchalitchi mwawo ndinso pa Radio Maria Malawi.

“Aliyense akalandira ubatizo amasanduka mtumiki wa Yesu Khristu,ana nawonso ndi atumiki akuyenera kutumikira malinga ndi msinkhu wawo,” anatero Bambo Mwakhwawa.

Pa mwambowu, mmodzi mwa ana Clara Chumba anapereka uthenga wake wa chaka cha utumiki wawo moyimira ana onse a mpingowu  m’dziko muno.

Uthengawu wati ana ndi kuwala kwa dziko lapansi,ndipo Ambuye Yesu Khristu ndi omwe amawawongolera pa moyo wawo wa uzimu.

“Ife ana tili ndi udindo wowalira ana anzathu amene adakali mu mdima wa machimo powaphunzitsa chikhalidwe choyera chomwe mpingo ndi makolo umatiphunzitsa kuti nafenso tiwalire ena,”anatero Clara.

Iye  watsindika kuti pali njira zina zoyipa zomwe zikufuna kuzimitsa nyali zawo monga kulekana ukwati kwa makolo, ziphunzitso zonama, kuwalemba ntchito ali achichepere, kuwaphunzitsa ufiti komanso nkhaza zochokera kwa makolo ngakhalenso kuwagwililira.

Chaka cha Utumiki wa ana chimachitika tsiku la chaka cha Epifania chaka chilichonse


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>