Akhristu a mparish ya St Martin Chirimba mu Archdayosizi ya Blantyre awapempha kuti adzipereke popititsa patsogolo moyo wa miphakati mparishiyi.
A Robert Msakambewa omwe ndi wapampando wa Parishiyi ndiwo alankhula izi kwa mtolankhani wathu pofotokozera momwe parish yi yayendetsera ntchito zake chaka changothachi.
A Msakambewa anati miphakati yakumana ndi mavuto ambiri kamba kakusapezeka kwa akhristu ake.
Iwo ati kudzera mu kafukufuku yemwe parishyi yachita, yapeza kuti akhristuwa akutanganidwa ndi zinthu monga zinkhoswe ndi zina zomwe zikulepheretsa kupititsa patsogolo miyoyo ya miphakati.
Iwo ati akhazikitsa njira zosiyanasiyana monga kuti misonkhano ya zochitika isamakhalepo tsiku lamulungu komanso kuyenda mmiphakati yonse ya parish yo.
Kupatula mavutowa parish yi ati zinthu zayenda bwino ku mbali ya chipembedzo, chitukuko komanso moyo wotukula ana.