Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi Walimbikitsa Akhristu a ku Mvunguti kuti Asafowoke

$
0
0

Episkopi wa dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Sitima, alimbikitsa akhristu aku Mvunguti mparishi ya Nankhwali mudayosiziyi,kuti asafowoke pa chikhristu chawo ngakhale akukumana ndi mavuto osiyanasiyana .

Ambuye Sitima atsimikizira akhristuwa, omwe kale ankapemphera ku tchalitchi cha St.Louis Monkey Bay kuti adziyenderedwa pafupipafupi,  pofuna kulimbikitsana nawo pa moyo wauzimu.

Akhristu akumalowo amakumana ndi mavuto aakulu maka a mayendedwe kamba koti amadalira maboti kuti adzilumikizana ndi anzawo aku tchalitchi cha St. Louis Monkey-Bay mparishiyo.

“Ndikulimbikitseni kuti ngakhale muli kutali ndi tchalitchi lanu koma mudziwe kuti tli nanu ndipo musafowoke pa chikhulupiliro chanu,”anatero Ambuye Stima.

Iwo ati mtsogolo muno akhristuwa akalimbikira ali ndi masophenya kuti adzawamangire nyumba yakuti azipempheleramo.

Pothilirapo ndemanga wapampando wa akhrisitu ampingowu kumalowa mayi Catherine Smart, ayamikira Ambuye Stima chifukwa chowayendera pofuna kuti adziwonere okha momwe anthuwo akukhalira pamoyo wawo wa uzimu.

Pakadali pano anthu amasonkhana pakhomo pa banja la bambo ndi mayi Smart akafuna kupemphera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>