Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akhristu Akuyenera Kukometsa Moyo Wawo wa Uzimu mu Chaka Chatsopanochi

$
0
0

Akhristu a mpingo wa katolika awapempha kuti pamene chaka chatsopano chayamba ayambiretu kutekeseka mu njira zosiyanasiyana pofuna kukometsa moyo wawo wauzimu.

Wansembe owona za utumiki mu Archdayosizi ya Blantyre, Bambo Alfred Chaima ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre.

Bambo Chaima ati akhristu a Katolika, amadziwika bwino ndi zinthu zina monga kulemekeza komanso kutsata makhalidwe a anthu oyera omwe iwo anawasankha kukhala nkhoswe zawo.

Iwo apempha akhristu kuti pamene chaka chatsopano chayamba, mkhristu aliyense akhale ofunitsitsa kutsata moyo wa oyera yemwe limana,tchalitchi,dayosizi kapena bungwe lawo la mu mpingo linasankha kukhala nkhoswe yawo.

Iwo apemphanso akhristu kuti ayesetse kuti chakachi chisanathe,akhale ndi mapemphero okumbukira nkhoswe yawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>