Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Wapampando wa Bungwe la AMECEA Asankhidwa Kukhala Kadinala

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francis, wakweza paudindo wampando wa  bungwe la maepiskopi a mdera kumvuma kwa Africa la AMECEA olemekezeka Ambuye Berhaneyesus Demerew Souraphiel kukhala kadinala.

Ambuye Souraphiel,omwenso ndi Episkopi wa Dayosizi ya Addis Ababa mdziko la Ethiopia, akwezedwa paudindowu limodzi ndi ma Arch-episkopi ena khumi ndi anayi ochokera mmayiko khumi ndi anayi pa dziko lonse.

Papa, akuyembekezeka kukhazikitsa maepiskopiwa kukhala makadinala loweruka pa 14 mwezi wa February.

Ambuye Souraphiel, anasankhidwa kukhala wapampando wa bungwe la AMECEA kulowa mmalo mwa Ark-episkopi wa archdayosizi ya Lilongwe olemekezeka Ambuye Tarcisius Ziyaye,pa msonkhano waukulu wa bungweli omwe unachitikira mu mzinda wa Lilongwe m’mwezi wa July chaka chatha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>