Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Stima wayamikira akhristu a mpingowu mu Dayosiziyi kamba kodzipeleka pothandiza mpingo mu njira zosiyanasiyana m’chaka changothachi.
Ambuye Stima alankhula izi pomwe amafotokozera mtolankhani wathu momwe dayosiziyi igwilire ntchito zake m’chaka cha 2015.
Iwo ati akhristu mu Dayosiziyi mchaka changothachi anadzipeleka kothelatu pothandiza mpingo wawo, zomwe ati zapeleka chilimbikitso chokwanira kuti chaka chino a khristuwa adziperekanso pa ntchito zawo zotukula mpingowu mu Dayosiziyi.
Pamenepa Ambuye Stima apempha anthu onse amene sanatengepo mbali mu chaka chapitachi kuti chaka chino ayesetse achitepo kanthu.