Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akhristu ndi Anthu Akufuna Kwabwino Apitirize Kuthandiza Radio Maria Malawi

$
0
0

Akhristu ndi anthu ena akufuna kwabwino m`dziko muno awapempha kuti athandize Radio Maria Malawi mu nyengo ino kuti ithe kupitiliza kutumikira anthu moyenera.

Wapampando wa Parish ya Mzedi mu Arkdayosizi ya Blantyre a Alfred Kamwendo ndiwo apereka pempholi pomwe parishiyi imapereka ndalama zokwana 100 thousand kwacha kuti ithandizire ntchito za wayilesiyi.

Iwo ati anawona kuti nkofunika kuti ayithandize wayilesiyi malinga ndi ntchito ya mtengo wapatali. imene ikugwira.

 A Kamwendo ati akuzindikira kuti munyengo ino chuma chimakhala chovuta  makamaka mmiyezi ya January ndi February komabe iwo ati akhristu akuyenerabe kuganizira wayilesiyi yomwe nayonso ikukumana ndi mavuto a zachuma kuti ipitilizebe kugwira ntchito zake.

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>