Nyumba ya malamulo mdziko la Canada yakhadzikitsa tsiku lachiwiri m’mwezi wa April chaka chilichonse kuti anthu mdzikolo, adzikumbulira mtsogoleri wakale wa mpingo wakatolika malemu Papa Yohane Paulo wachiwiri Oyera.
Lamulo lokhazikitsira tsikuli, likutsindikanso kuti malemu Papa Yohane Paulo wachiwiri Oyera, akuyenera kulemekezedwa ngati katswiri yemwe amalemekeza ulemelero wa anthu komanso kulimbikitsa ufulu pakati pa anthu.
Papa Yohane Paulo Wachiwiri Oyera, anamwalira pa 2 April mchaka cha 2005, ndipo patha zaka khumi tsopano chimwalilire cha Papayu.