Munthu m’modzi wafa ndipo ena atatu akuti avulala ndi madzi osefukira mu m’tsinje wa Likangala m’boma la Zomba.
Malinga ndi Wofalitsa nkhani za apolisi m`boma la Zomba Constable Patricio Supliano ati, madzi a mphamvu ochokera ku mtunda kwa mtsinjewu anabwera ochuluka ndipo munthu mmodzi ndi yemwe wamwalira atakokololedwa ndi madziwa ali mnyumba mwake, ndipo ana ena atatu avulala kwambiri chifukwa cha madziwo, ndipo akulandira chithandizo pa chipatala chachikulu cha Zomba.
Madziwa awononga kwambiri nyumba komanso katundu wosiyanasiyana.Mtsinje wa Likangala ku Zomba wadutsa midzi ya Sadzi, Namalaka komanso MPondabwino.