Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco lamulungu lomwe ndi tsiku la chaka cha Ubatizo wa Ambuye Yesu Khristu, wapereka Sacrament la Ubatizo kwa ana makumi atatu ndi atatu {33}.
Papa Francisco wapereka Sacrament-li kwa ana khumi ndi awiri omwe ndi aamuna ndipo ana makumi awiri ndi mmodzi omwe ndi aakazi, omwe ndi ana a anthu ogwira ntchito ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Chaka cha Ubatizo wa Ambuye Yesu chomwe chimachitika pambuyo pa sabata ziwiri za nyengo ya khirisimasi ndi chomwenso chimatseka chikondwererochi ndi kutsekulira nyengo ya pa chaka cha mpingo.